Nsembe. Nkhondo. Mayesero. Chiwembu. Chiyembekezo. Chipulumutso.
Mulungu anasankha kudzivumbulutsa yekha kwa anthu, osati kudzera mu mfundo zokhazikika chabe, kapena m’nzeru chabe, kapenanso m’ziphunzitso chabe, koma makamaka kudzera m’nkhani za uneneri, nkhondo, chifundo, chiweruzo, zozizwitsa, imfa, moyo, ndi chikhululukiro. Nkhani ya mmene Mulungu anakonzera kupulumutsa anthu yafotokozedwa mwatsatanetsatane kuchokera m’buku la Genesis mpaka Chivumbulutso.
Buku limeneli limakuthandizani kudziwa mwatsatenetsatane nkhani yonse ya m’Baibulo mosavuta. Limaonetsa nkhani zikukuzikulu m’njira yosavuta kutsatira yonga ngati sewero.
Werengani tsopano!